bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.94 kB
JSON
["Ndipo kunali atapita masiku, nyengo ya kucheka tirigu Samisoni anakacheza ndi mkazi wake ndi kumtengera mwanawambuzi, nati, Ndidzalowa kwa mkazi wanga kuchipinda. Koma atate wake sanamlole kulowamo.","Nati atate wake, Ndinanenetsa kuti umuda konse, potero ndinampereka kwa bwenzi lako; mng'ono wake sakoma koposa iye nanga? Ukhale naye, m'malo mwa winayu.","Koma Samisoni, ananena nao, Nthawi yino ndikhala wosapalamula pa Afilisti, powachitira choipa ine.","Namuka Samisoni, nagwira ankhandwe mazana atatu, natenga miuni, nalunza michira, naika muuni pakati pa michira iwiri iliyonse.","Nayatsa miuni, nawataya ku tirigu wosacheka wa Afilisti, natentha miulu, ndi tirigu wosacheka yemwe, ndi minda ya azitona yomwe.","Pamenepo Afilisti anati, Wachita ichi ndani? Nati, Samisoni mkamwini wa munthuyo wa ku Timna, popeza analanda mkazi wake, nampereka kwa mnzake. Pamenepo Afilisti anakwera namtentha mkaziyo ndi atate wake ndi moto.","Ndipo Samisoni ananena nao, Mukatero ndidzakubwezerani chilango ndi pamenepo ndidzaleka.","Ndipo anawakantha nyung'unyu ndi ntchafu, makanthidwe akulu; natsika nakhala m'phanga mwa thanthwe la ku Etamu.","Pamenepo Afilisti anakwera, namanga misasa m'Yuda, natandika m'Lehi.","Ndipo anthu a Yuda anati, Mwatikwerera chifukwa ninji? Nati iwo, Takwera kumanga Samisoni, kumchitira iye monga anatichitira ife.","Pamenepo anatsikira ku phanga la Etamu amuna zikwi zitatu a ku Yuda, nati kwa Samisoni, Sudziwa kodi kuti Afilisti ndiwo akutilamulira ife? Nchiyani ichi watichitira? Nati iye kwa iwowa, Monga anandichitira ine ndawachitira iwo.","Ndipo ananena naye, Tatsika ife tikumange, kuti tikupereke m'dzanja la Afilisti, Nanena nao Samisoni, Mundilumbirire kuti simudzandigwera nokha.","Ndipo anati kwa iye, Iai, koma kumanga tidzakumanga, ndi kukupereka m'dzanja lao; koma kupha sitikupha iwe. Nammanga iye ndi zingwe ziwiri zatsopano, nakwera naye kuchokera kuthanthwe.","Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.","Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.","Nati Samisoni,Ndi chibwano cha bulu, miulumiulu,amuna chikwi ndawakantha ndi chibwano cha bulu.","Ndipo kunali, atatha kunena, anataya chibwano m'dzanja lake; nawatcha malowo Ramatilehi ndiko kunena chitunda cha chibwano.","Ndipo anamva ludzu lambiri, naitana kwa Yehova, nati, Mwapatsa Inu chipulumutso ichi chachikulu ndi dzanja la kapolo wanu; ndipo kodi ndife nalo ludzu tsopano ndi kugwa m'dzanja la osadulidwa awa?","Pamenepo Mulungu anang'amba pokumbika paja pa Lehi, natulukamo madzi; namwa iye, nubwera moyo wake, natsitsimuka iye; chifukwa chake anawatcha dzina lake, Kasupe wa wofuula, ndiwo m'Lehi mpaka lero lino.","Ndipo Samisoni anaweruza Israele m'masiku a Afilisti zaka makumi awiri."]