UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.06 kB
["Pamenepo amuna a Efuremu analalikidwa, napita kumpoto; nati kwa Yefita, Wapitiriranji kuthira nkhondo ana a Amoni, osatiitana ife timuke nawe? Tidzakutenthera nyumba yako ndi moto pamtu pako.","Ndipo Yefita anati kwa iwo, Ine ndi anthu anga tinatsutsana kwakukulu ndi ana a Amoni, koma pamene ndinakuitanani inu simunandipulumutsa m'dzanja lao.","Ndipo pakuona ine kuti simundipulumutsa, ndinataya moyo wanga ndi kupita kwa ana a Amoni; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja langa; mwakwereranji tsono lero lino kundichitira nkhondo?","Pamenepo Yefita anamemeza amuna onse a m'Giliyadi nalimbana naye Efuremu; ndipo amuna a Giliyadi anakantha Efuremu, chifukwa adati, Inu Agiliyadi ndinu akuthawa Efuremu, pakati pa Efuremu ndi pakati pa Manase.","Ndipo Agiliyadi anatsekereza madooko a Yordani a Efuremu; ndipo kunatero kuti, akati othawa a Efuremu, Ndioloke, amuna a Giliyadi anati kwa Iye, Ndiwe Mwefuremu kodi? Akati, Iai;","pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.","Ndipo Yefita anaweruza Israele zaka zisanu ndi chimodzi; nafa Yefita Mgiliyadi, naikidwa m'mudzi wina wa Giliyadi.","Ndi pambuyo pake Ibizani wa ku Betelehemu anaweruza Israele.","Ndipo anali nao ana amuna makumi atatu; ndi ana akazi makumi atatu anawakwatitsa kwina, natengera ana ake amuna ana akazi makumi atatu ochokera kwina. Ndipo anaweruza Israele zaka zisanu ndi ziwiri.","Nafa Ibizani naikidwa ku Betelehemu.","Ndi pambuyo pake Eloni Mzebuloni anaweruza Israele; naweruza Israele zaka khumi.","Nafa Eloni Mzebuloni naikidwa m'Ayaloni m'dziko la Zebuloni.","Ndi pambuyo pake Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni anaweruza Israele.","Ndipo anali nao ana amuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.","Nafa Abidoni mwana wa Hilele wa ku Piratoni, naikidwa m'Piratoni m'dziko la Efuremu ku mapiri a Amaleke."]