bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.45 kB
JSON
["Ndipo ndinaona chizindikiro china m'mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa, angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.","Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosanganiza ndi moto; ndipo iwo amene anachilaka chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.","Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.","Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.","Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kachisi wa chihema cha umboni m'Mwamba:","ndipo anatuluka m'Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.","Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.","Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa m'Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri."]