bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.37 kB
JSON
["Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,","Nena ndi ana a Israele ndi kuti, Mudziikire midzi yopulumukirako, monga ndinanena kwa inu mwa dzanja la Mose.","Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.","Munthu akathawira umodzi wa midzi iyi, aziima polowera pa chipata cha mudziwo, nafotokozere mlandu wake m'makutu a akulu a mudziwo; pamenepo azimlandira kumudzi kwao, ndi kumpatsa malo, kuti akhale pakati pao.","Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.","Ndipo azikhala m'mudzimo mpaka adzaima pamaso pa msonkhano anene mlandu wake, mpaka atafa mkulu wa ansembe wa m'masiku omwewo; pamenepo wakupha mnzake azibwerera ndi kufika kumudzi kwake, ndi nyumba yake, kumudzi kumene adathawako.","Ndipo anapatula Kedesi m'Galileya ku mapiri a Nafutali, ndi Sekemu ku mapiri a Efuremu, ndi mudzi wa Ariba ndiwo Hebroni ku mapiri a Yuda.","Ndipo tsidya lija la Yordani kum'mawa kwa Yeriko, anaika Bezeri m'chipululu, kuchidikha, wa fuko la Rubeni, ndi Ramoti m'Giliyadi wa fuko la Gadi, ndi Golani m'Basani wa fuko la Manase.","Iyi ndi midzi yoikidwira ana onse a Israele, ndi mlendo wakukhala pakati pao kuti athawireko aliyense wakupha munthu, ndi kuti asafe ndi dzanja la wolipsa mwazi, asanaime pamaso pa msonkhano."]