UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 4.99 kB
["Ndipo maere achiwiri anamtulukira Simeoni, fuko la ana a Simeoni monga mwa mabanja ao; ndi cholowa chao chinali pakati pa cholowa cha ana a Yuda.","Ndipo anali nacho cholowa chao Beereseba, kapena Sheba, ndi Molada;","ndi Hazara-Suwala, ndi Bala, ndi Ezemu;","ndi Elitoladi, ndi Betuli, ndi Horoma;","ndi Zikilagi, ndi Betemara-Kaboti, ndi Hazara-Susa:","ndi Betelebaoti, ndi Saruheni; midzi khumi ndi itatu ndi milaga yao;","Aini, Rimoni ndi Eteri ndi Asani; midzi inai ndi milaga yao;","ndi milaga yonse yozungulira midzi iyi mpaka Baalati-Bere ndiwo Rama kumwera. Ndicho cholowa cha fuko la ana a Simeoni, monga mwa mabanja ao.","M'gawo la ana a Yuda muli cholowa cha ana a Simeoni; popeza gawo la ana a Yuda linawachulukira; chifukwa chake ana a Simeoni anali nacho cholowa pakati pa cholowa chao.","Ndipo maere achitatu anakwerera ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao; ndi malire a cholowa chao anafikira ku Saridi;","nakwera malire ao kunka kumadzulo ndi ku Mareyala nafikira ku Dabeseti, nafikira ku mtsinje wa patsogolo pa Yokoneamu;","ndi kuchokera ku Saridi anazungulira kunka kum'mawa kumatulukira dzuwa, mpaka malire a Kisiloti-Tabori; natuluka kunka ku Daberati, nakwera ku Yafiya;","ndi pochoka pamenepo anapitirira kunka kum'mawa ku Gatihefere, ku Etikazini; natuluka ku Rimoni umene ulembedwa mpaka ku Neya,","nauzungulira malire kumpoto, kunka ku Hanatoni; ndi matulukiro ake anali ku chigwa cha Ifutahele;","ndi Katati, ndi Nahalala ndi Simironi, ndi Idala ndi Betelehemu: midzi khumi ndi iwiri ndi milaga yao.","Ichi ndi cholowa cha ana a Zebuloni monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.","Maere achinai anamtulukira Isakara, kunena za ana a Isakara monga mwa mabanja ao.","Ndi malire ao anali ku Yezireele, ndi Kesuloti, ndi Sunemu;","ndi Hafaraimu, ndi Siyoni, ndi Anaharati;","ndi Rabiti ndi Kisiyoni, ndi Ebezi;","ndi Remeti ndi Enganimu ndi Enihada, ndi Betepazezi;","ndi malire anafikira ku Tabori, ndi Sahazuma, ndi Betesemesi; ndi matulukiro a malire ao anali ku Yordani; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi ndi milaga yao.","Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Isakara, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao.","Ndipo maere achisanu analitulukira fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao.","Ndi malire ao ndiwo Helekati, ndi Hali, ndi Beteni ndi Akisafu;","ndi Alamumeleki, ndi Amada, ndi Misala; nafikira ku Karimele kumadzulo ndi ku Sihori-Libinati;","nazungulira kotulukira dzuwa ku Betedagoni, nafikira ku Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifutahele, kumpoto ku Betemeke, ndi Neiyeli; natulukira ku Kabulu kulamanzere,","ndi Ebroni, ndi Rehobu, ndi Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni wamkulu;","nazungulira malire kunka ku Rama, ndi kumudzi wa linga la Tiro; nazungulira malire kunka ku Hosa; ndi matulukiro ake anali kunyanja, kuchokera ku Mahalabu mpaka ku Akizibu;","Uma womwe ndi Afeki, ndi Rehobu; midzi makumi awiri mphambu iwiri ndi milaga yao.","Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Asere monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.","Maere achisanu ndi chimodzi anatulukira ana a Nafutali, ana a Nafutali monga mwa mabanja ao.","Ndipo malire ao anayambira ku Helefe ku thundu wa ku Zaananimu, ndi Adami-Nekebu, ndi Yabinele, mpaka ku Lakumu; ndi matulukiro ake anali ku Yordani;","nazungulira malire kunka kumadzulo ku Azinoti-Tabori, natulukira komweko kunka ku Hukoku; nafikira ku Zebuloni kumwera, nafikira ku Asere kumadzulo, ndi ku Yuda pa Yordani kum'mawa.","Ndipo midzi yamalinga ndiyo Zidimu, Zeri, ndi Hamati, Rakati, ndi Kinereti;","ndi Adama, ndi Rama, ndi Hazori;","ndi Kedesi, ndi Ederei, ndi Enihazori;","ndi Yironi, ndi Migidalele, Horemu, ndi Betanati, ndi Betesemesi; midzi khumi ndi isanu ndi inai, ndi milaga yao.","Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Nafutali, monga mwa mabanja ao, midzi ndi milaga yao.","Maere achisanu ndi chiwiri anatulukira fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao.","Ndipo malire a cholowa chao anali Zora, ndi Esitaoli, ndi Irisemesi;","Saalabini, ndi Ayaloni ndi Itila;","ndi Eloni ndi Timna ndi Ekeroni;","ndi Eliteke, ndi Gibetoni, ndi Baalati;","ndi Yehudi, ndi Beneberaki, ndi Gatirimoni;","ndi Meyarikoni, ndi Rakoni, ndi malire pandunji pa Yopa.","Koma malire a ana a Dani anatuluka kupitirira iwowa; pakuti ana a Dani anakwera nathira nkhondo ku Lesemu, naulanda naukantha ndi lupanga lakuthwa, naulandira, nakhala m'mwemo, nautcha Lesemu, Dani; ndilo dzina la Dani atate wao.","Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Dani, monga mwa mabanja ao, midzi iyi ndi milaga yao.","Ndipo atatha kuligawa dziko likhale cholowa chao monga mwa malire ake, ana a Israele anapatsa Yoswa mwana wa Nuni cholowa pakati pao;","monga mwa lamulo la Yehova anampatsa mudzi umene anawapempha, ndiwo Timnati-Sera, ku mapiri a Efuremu; ndipo anamanga mudziwo nakhala m'mwemo.","Izi ndizo zolowa anazigawa Eleazara wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele, zikhale zaozao, ndi kulota maere ku Silo pamaso pa Yehova ku khomo la chihema chokomanako. Momwemo anatha kuligawa dziko."]