bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 5.63 kB
JSON
["Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.","Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;","natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;","napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.","Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;","nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;","nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;","nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.","Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumidzi ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.","Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;","natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.","Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.","Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.","Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.","Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere.","Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake.","Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.","Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pa bulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?","Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.","Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.","Ndipo midzi ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;","ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;","ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani;","Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;","ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori;","Amama ndi Sema ndi Molada;","ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti;","ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya;","Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu;","ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma;","ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana;","ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi milaga yao.","Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;","ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu;","Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;","ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yao.","Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi;","ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;","Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;","ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi;","ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.","Libina ndi Eteri ndi Asani;","ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu;","ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.","Ekeroni pamodzi ndi midzi yake ndi milaga yao;","kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi milaga yao.","Asidodi, midzi yake ndi milaga yake; Gaza, midzi yake ndi milaga yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.","Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko;","ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri;","ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu;","ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.","Arabu, ndi Duma, ndi Esani;","ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka;","ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.","Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;","ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;","Kaini, Gibea ndi Timna; midzi khumi pamodzi ndi milaga yao.","Halahulu, Betezuri, ndi Gedori,","ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.","Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi milaga yao.","M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka;","ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mchere, ndi Engedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.","Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino."]