bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.82 kB
JSON
["Ndipo chingakhale chipangano choyambachi chinali nazo zoikika za kulambira, ndi malo opatulika a pa dziko lapansi.","Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.","Koma m'kati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa Malo Opatulika kwambiri;","okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo, ndi magome a chipangano;","ndi pamwamba pake akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo; za izi sitikhoza kunena tsopano paderapadera.","Ndipo izi zitakonzeka kotero, ansembe amalowa m'chihema choyamba kosalekeza, ndi kutsiriza kulambirako;","koma kulowa m'chachiwiri, mkulu wa ansembe yekha kamodzi pachaka, wosati wopanda mwazi, umene apereka chifukwa cha iye yekha, ndi zolakwa za anthu;","Mzimu Woyera wodziwitsa nako, kuti njira yolowa nayo kumalo opatulika siinaonetsedwe, pokhala chihema choyamba chili chilili;","ndicho chiphiphiritso cha kunthawi yomweyi, m'mene mitulo ndi nsembenso zinaperekedwa zosakhoza, ponena za chikumbu mtima, kuyesa wangwiro wolambirayo.","Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.","Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza mwa, chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi,","kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.","Pakuti ngati mwazi wa mbuzi ndi ng'ombe zamphongo, ndi makala a ng'ombe yamthandi owazawaza pa iwo odetsedwa, upatutsa kufikira chiyeretso cha thupi;","koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?","Ndipo mwa ichi ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zolowa zosatha.","Pakuti pamene pali chopangiratu pafunika pafike imfa ya wolemberayo.","Pakuti chopangiratu chiona mphamvu atafa mwini wake; popeza chilibe mphamvu konse pokhala wolemberayo ali ndi moyo;","momwemo choyambachonso sichinakonzeka chopanda mwazi.","Pakuti pamene Mose adalankhulira anthu onse lamulo lililonse monga mwa chilamulo, anatenga mwazi wa anaang'ombe ndi mbuzi, pamodzi ndi madzi ndi ubweya wofiira ndi hisope, nawaza buku lomwe, ndi anthu onse,","nati, Uwu ndi mwazi wa chipangano Mulungu adakulamulani.","Ndiponso chihema ndi zotengera zonse za utumikiro anaziwaza momwemo ndi mwaziwo.","Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.","Pomwepo padafunika kuti zifaniziro za zinthu za m'Mwamba ziyeretsedwe ndi izi; koma zam'mwamba zenizeni ziyeretsedwe ndi nsembe zoposa izi.","Pakuti Khristu sanalowa m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu m'Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;","kosati kuti adzipereke yekha kawirikawiri; monga mkulu wa ansembe alowa m'malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake;","chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.","Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro;","kotero Khristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso."]