bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.5 kB
JSON
["Ndidandaulira tsono, poyambayamba, kuti achitike mapembedzo, mapemphero, mapembedzero, mayamiko, chifukwa cha anthu onse;","chifukwa cha mafumu ndi onse akuchita ulamuliro; kuti m'moyo mwathu tikakhale odika mtima ndi achete m'kulemekeza Mulungu, ndi m'kulemekezeka monse.","Pakuti ichi nchokoma ndi cholandirika pamaso pa Mulungu Mpulumutsi wathu;","amene afuna anthu onse apulumuke, nafike pozindikira choonadi.","Pakuti pali Mulungu mmodzi, ndi Mtetezi mmodzi pakati pa Mulungu ndi anthu, ndiye munthu, Khristu Yesu,","amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake;","umene anandiika ine mlaliki wake ndi mtumwi (ndinena zoona, wosanama ine), mphunzitsi wa amitundu m'chikhulupiriro ndi choonadi.","Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.","Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;","komatu (umo mokomera akazi akuvomereza kulemekeza Mulungu), mwa ntchito zabwino.","Mkazi aphunzire akhale wachete m'kumvera konse.","Koma sindilola ine kuti mkazi aphunzitse, kapena kulamulira mwamuna; komatu akhale chete.","Pakuti Adamu anayamba kulengedwa, pamenepo Heva;","ndipo Adamu sananyengedwa, koma mkaziyo ponyengedwa analowa m'kulakwa;","koma adzapulumutsidwa mwa kubala mwana, ngati akhala m'chikhulupiriro ndi chikondi ndi chiyeretso pamodzi ndi chidziletso."]