UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.88 kB
["Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;","ndi kuti tilanditsidwe m'manja a anthu osayenera ndi oipa; pakuti si onse ali nacho chikhulupiriro.","Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;","koma tikhulupirira mwa Ambuye za inu, kuti mumachita, ndiponso mudzachita zimene tikulamulirani.","Ndipo Ambuye atsogolere bwino mitima yanu ilowe m'chikondi cha mulungu ndi m'chipiriro cha Khristu.","Ndipo tikulamulirani, abale, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti mubwevuke kwa mbale yense wakuyenda dwakedwake, wosatsata mwambo umene anaulandira kwa ife.","Pakuti mudziwa nokha m'mene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwakedwake mwa inu;","kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu aliyense, komatu m'chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu;","si chifukwa tilibe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.","Pakutinso pamene tinali nanu tidakulamulirani ichi, Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.","Pakuti tikumva za ena mwa inu kuti ayenda dwakedwake, osagwira ntchito konse, koma ali ochita mwina ndi mwina.","Koma oterewa tiwalamulira ndi kuwadandaulira mwa Ambuye Yesu Khristu, kuti agwire ntchito pokhala chete, nadye chakudya cha iwo okha.","Koma inu, abale, musaleme pakuchita zabwino.","Koma ngati wina samvera mau athu m'kalata uyu, yang'anirani ameneyo, kuti musayanjane naye, kuti achite manyazi.","Koma musamuyese mdani, koma mumuyambirire ngati mbale.","Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.","Ndipereka moni ndi dzanja langa Paulo; ndicho chizindikiro m'kalata aliyense; ndiko kulemba kwanga.","Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse."]