UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.2 kB
["Ndipo tikupemphani, abale, chifukwa cha kudza kwake kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi kusonkhana pamodzi kwathu kwa Iye;","kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;","munthu asakunyengeni konseko; kuti silifika, koma chiyambe chifike chipatukocho, navumbulutsike munthu wosaweruzika, mwana wa chionongeko,","amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.","Simukumbukira kodi, kuti pokhala nanu, ndisanachoke ine, ndinakuuzani izi?","Ndipo tsopano chomletsa muchidziwa, kuti akavumbulitsidwe iye m'nyengo yake ya iye yekha.","Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.","Ndipo pamenepo adzavumbulutsidwa wosaweruzikayo, amene Ambuye Yesu adzamthera ndi mzimu wa pakamwa pake, nadzamuononga ndi maonekedwe a kudza kwake;","ndiye amene kudza kwake kuli monga mwa machitidwe a Satana, mu mphamvu yonse, ndi zizindikiro ndi zozizwa zonama;","ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandira, kuti akapulumutsidwe iwo.","Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;","kuti aweruzidwe onse amene sanakhulupirira choonadi, komatu anakondwera ndi chosalungama.","Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;","kumene anaitanako inu mwa Uthenga Wabwino wathu, kuti mulandire ulemerero wa Ambuye wathu Yesu Khristu.","Chifukwa chake tsono, abale, chilimikani, gwiritsani miyambo imene tinakuphunzitsani, kapena mwa mau, kapena mwa kalata wathu.","Ndipo Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi Mulungu Atate wathu amene anatikonda natipatsa chisangalatso chosatha ndi chiyembekezo chokoma mwa chisomo,","asangalatse mitima yanu, nakhazikitse inu mu ntchito yonse ndi mau onse abwino."]