bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.63 kB
JSON
["Paulo, ndi Silivano, ndi Timoteo, kwa Mpingo wa Atesalonika mwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu:","Chisomo kwa inu ndi mtendere wa kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.","Tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale, monga kuyenera; pakuti chikhulupiriro chanu chikula chikulire, ndipo chichulukira chikondano cha inu nonse, yense pa mnzake;","kotero kuti ife tokha tidzitamandira za inu m'Mipingo ya Mulungu, chifukwa cha chipiriro chanu, ndi chikhulupiriro chanu, m'mazunzo anu onse ndi zisautsozo muzimva;","ndicho chitsimikizo cha chiweruziro cholungama cha Mulungu; kuti mukawerengedwe oyenera ufumu wa Mulungu, umenenso mumvera zowawa;","popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso,","ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,","m'lawi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Ambuye wathu Yesu;","amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake,","pamene adzadza kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ake, ndi kukhala wodabwizitsa mwa onse akukhulupirira (popeza munakhulupirira umboni wathu wa kwa inu) m'tsiku lija.","Kukatero tikupemphereraninso nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akakuyeseni inu oyenera kuitanidwa kwanu, nakakwaniritse chomkomera chonse, ndi ntchito ya chikhulupiriro mumphamvu;","kuti dzina la Ambuye wathu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mwa Iye, monga mwa chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu."]