bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.79 kB
JSON
["Pamene mutuluka pa mdani wanu kunkhondo, ndi kuona akavalo ndi magaleta ndi anthu akuchulukira inu, musawaopa; popeza Yehova Mulungu wanu, amene anakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ali ndi inu.","Ndipo kudzali, pamene muyandikiza kunkhondo, ayandikize wansembe nanene ndi anthu,","nati nao, Tamverani, Israele, muyandikiza kunkhondo lero pa adani anu; musafumuka mitima yanu; musachita mantha, kapena kunjenjemera, kapena kuopsedwa pamaso pao;","pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye wakumuka nanu, kugwirira inu pa adani anu, kukupulumutsani.","Ndipo akapitao anene ndi anthu, ndi kuti, Ndani munthuyo anamanga nyumba yatsopano, osalowamo? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo nangalowemo munthu wina.","Ndipo ndani munthuyo anaoka munda wamphesa osalawa zipatso zake? Amuke nabwerere kunyumba yake, kuti angafe kunkhondo, nangalawe munthu wina zipatso zake.","Ndipo munthuyo ndani anapala bwenzi ndi mkazi osamtenga? Amuke nabwerere kunyumba kwake, kuti angafe kunkhondo, nangamtenge munthu wina.","Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakuchita mantha ndi wofumuka mtima? Amuke nabwerere kunyumba kwake, ingasungunuke mitima ya abale ake monga mtima wake.","Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.","Pamene muyandikiza mudzi kuchita nao nkhondo, muziufuulira ndi mtendere.","Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opereka m'mwemo akhale akapolo anu, nadzakugwirirani ntchito yathangata.","Koma ukapanda kuchita zamtendere ndi inu, koma kuchita nkhondo nanu, pamenepo muumangire tsasa.","Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m'dzanja lanu, mukanthe amuna ake onse ndi lupanga lakuthwa.","Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mudzimo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.","Muzitero nayo midzi yonse yokhala kutalitali ndi inu, yosakhala midzi ya amitundu awa.","Koma za midzi ya amitundu awa, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ikhale cholowa chanu, musasiyepo chamoyo chilichonse chakupuma;","koma muwaononge konse Ahiti, ndi Aamori, Akanani, ndi Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi; monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani;","kuti angakuphunzitseni kuchita monga mwa zonyansa zao zonse, amazichitira milungu yao; ndipo mungachimwire Yehova Mulungu wanu.","Pamene mumangira tsasa mudzi masiku ambiri, pouthirira nkhondo kuugwira, usamaononga mitengo yake ndi kuitema ndi nkhwangwa; pakuti ukadyeko, osailikha; pakuti mtengo wa m'munda ndiwo munthu kodi kuti uumangire tsasa?","Koma mitengo yoidziwa inu kuti si ndiyo mitengo yazipatso, imeneyi muiononge ndi kuilikha; ndipo mudzi wochita nanu nkhondo muumangire machemba, mpaka mukaugonjetsa."]