bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.7 kB
JSON
["Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:","Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.","Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;","monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.","Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,","kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.","Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,","chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi chisamaliro.","Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,","kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.","Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake;","kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.","Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,","ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.","Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,","sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga;","kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;","ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,","ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba,","imene anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m'zakumwamba,","pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;","ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Mpingo","amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse."]