UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 7.33 kB
["Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?","Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani;","nati kwa iye, Tuluka kudziko lako ndi kwa abale ako, ndipo tiye kudziko limene ndidzakusonyeza iwe.","Pamenepo anatuluka m'dziko la Akaldeya namanga m'Harani: ndipo, kuchokera kumeneko, atamwalira atate wake, Mulungu anamsuntha alowe m'dziko lino, m'mene mukhalamo tsopano;","ndipo sanampatsa cholowa chake m'menemo, ngakhale popondapo phazi lake iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lake, ndi la mbeu yake yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.","Koma Mulungu analankhula chotero, kuti mbeu yake idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawachititsa ukapolo, nadzawachitira choipa, zaka mazana anai.","Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzatuluka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.","Ndipo anampatsa iye chipangano cha mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isaki, namdula tsiku lachisanu ndi chitatu; ndi Isaki anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.","Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Ejipito; ndipo Mulungu anali naye,","namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.","Koma inadza njala pa Ejipito ndi Kanani lonse, ndi chisautso chachikulu; ndipo sanapeza chakudya makolo athu.","Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Ejipito, anatuma makolo athu ulendo woyamba.","Ndipo pa ulendo wachiwiri Yosefe anazindikirika ndi abale ake; ndipo fuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.","Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wake, ndi a banja lake lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.","Ndipo Yakobo anatsikira ku Ejipito; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;","ndipo anawanyamula kupita nao ku Sekemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wake wa ndalama kwa ana a Hamori m'Sekemu.","Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka m'Ejipito,","kufikira inauka mfumu ina pa Ejipito, imene siinamdziwa Yosefe.","Imeneyo inachenjerera fuko lathu, niwachitira choipa makolo athu, niwatayitsa tiana tao, kuti tingakhale ndi moyo.","Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake:","ndipo pakutayika iye, anamtola mwana wamkazi wa Farao, namlera akhale mwana wake.","Ndipo Mose anaphunzira nzeru zonse za Aejipito; nali wamphamvu m'mau ake ndi m'ntchito zake.","Koma pamene zaka zake zinafikira ngati makumi anai, kunalowa mumtima mwake kuzonda abale ake ana a Israele.","Ndipo pakuona wina woti alikumchitira choipa, iye anamtchinjiriza, nambwezera chilango wozunzayo, nakantha Mwejipito.","Ndipo anayesa kuti abale ake akazindikira kuti Mulungu alikuwapatsa chipulumutso mwa dzanja lake; koma sanazindikira.","Ndipo m'mawa mwake anawaonekera alikulimbana ndeu, ndipo anati awateteze, ayanjanenso, nati, Amuna inu, muli abale; muchitirana choipa bwanji?","Koma iye wakumchitira mnzake choipa anamkankha, nati, Wakuika iwe ndani mkulu ndi wotiweruzira?","Kodi ufuna kundipha ine, monga muja unapha Mwejipito dzulo?","Ndipo Mose anathawa pa mau awa, nakhala mlendo m'dziko la Midiyani; kumeneko anabala ana amuna awiri.","Ndipo zitapita zaka makumi anai, anamuonekera mngelo m'chipululu cha Sinai, m'lawi la moto wa m'chitsamba.","Koma Mose pakuona, anazizwa pa choonekacho; ndipo pakuyandikira iye kukaona, kunadza mau a Ambuye,","akuti, Ine ndine Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, ndi wa Isaki, ndi wa Yakobo. Ndipo Mose ananthunthumira, osalimbika mtima kupenyetsako.","Ndipo Ambuye anati kwa iye, Masula nsapato kumapazi ako; pakuti pa malo amene upondapo mpopatulika.","Kuona ndaona choipidwa nacho anthu anga ali m'Ejipito, ndipo amva kubuula kwao; ndipo ndatsika kuwalanditsa; ndipo tsopano, tiye kuno, ndikutume ku Ejipito.","Mose uyu amene anamkana, ndi kuti, Wakuika iwe ndani mkulu ndi woweruza? Ameneyo Mulungu anamtuma akhale mkulu, ndi mombolo, ndi dzanja la mngelo womuonekera pachitsamba.","Ameneyo anawatsogolera, natuluka nao atachita zozizwa ndi zizindikiro m'Ejipito, ndi m'Nyanja Yofiira, ndi m'chipululu zaka makumi anai.","Uyu ndi Mose uja adati kwa ana a Israele, Mulungu adzakuutsirani Mneneri wa mwa abale anu, monga ine.","Uyu ndiye amene anali mu Mpingo m'chipululu pamodzi ndi mngelo wakulankhula naye m'phiri la Sinai, ndi makolo athu: amene analandira maneno amoyo akutipatsa ife;","amene makolo athu sanafuna kumvera iye, koma anamkankha achoke, nabwerera m'mbuyo mumtima mwao ku Ejipito,","nati ndi Aroni, Tipangireni milungu yotitsogolera ife; pakuti Mose uja, amene anatitulutsa m'Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.","Ndipo anapanga mwanawang'ombe masiku omwewo, nabwera nayo nsembe kwa fanolo, nasekerera ndi ntchito za manja ao.","Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri,Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembezaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?","Ndipo munatenga chihema cha Moleki,ndi nyenyezi ya mulungu Refani,zithunzizo mudazipanga kuzilambira;ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.","Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.","Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;","amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.","Koma Solomoni anammangira nyumba.","Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,","Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga,ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga.Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye,kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?","Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?","Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.","Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;","inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunga.","Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.","Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,","nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.","Koma anafuula ndi mau akulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;","ndipo anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.","Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.","Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo."]