bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 5 kB
JSON
["Ndipo analowa, napyola pa Yeriko.","Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma.","Ndipo anafuna kuona Yesu ndiye uti, ndipo sanathe, chifukwa cha khamulo, pakuti anali wamfupi msinkhu.","Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi.","Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.","Ndipo anafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera.","Ndipo m'mene anachiona anadandaula onse, nanena, Analowa amchereze munthu ali wochimwa.","Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.","Ndipo Yesu anati kwa iye, Lero chipulumutso chagwera nyumba iyi, popeza iyenso ndiye mwana wa Abrahamu.","Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.","Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo.","Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako.","Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso.","Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nizituma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.","Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda.","Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi.","Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.","Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu.","Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu.","Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu;","pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa.","Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiika, ndi wotuta chimene sindinachifesa;","ndipo sunapereka bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake?","Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi.","Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi.","Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa.","Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.","Ndipo m'mene adanena izi anawatsogolera nakwera ku Yerusalemu.","Ndipo kunali, m'mene anayandikira ku Betefage ndi Betaniya, pa phiri lotchedwa la Azitona, anatuma awiri a ophunzira,","nati, Mukani kumudzi uli pandunji panu; m'menemo, polowa, mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, pamenepo palibe munthu anakwerapo nthawi iliyonse; mummasule iye nimumtenge.","Ndipo munthu akati kwa inu, Mummasuliranji? Mudzatero naye, Ambuye amfuna iye.","Ndipo anachoka otumidwawo, napeza monga adanena kwa iwo.","Ndipo pamene anamasula mwana wa bulu, eni ake anati kwa iwo, Mumasuliranji mwana wa bulu?","Ndipo anati, Ambuye amfuna iye.","Ndipo anadza naye kwa Yesu; ndipo anayalika zovala zao pa mwana wa buluyo, nakwezapo Yesu.","Ndipo pakupita Iye, anayala zovala zao m'njira.","Ndipo pakuyandikira Iye tsono potsetsereka pake pa phiri la Azitona, unyinji wonse wa ophunzira anayamba kukondwera ndi kuyamika Mulungu ndi mau akulu, chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu anaziona;","nanena, Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m'dzina la Ambuye; mtendere m'Mwamba, ndi ulemerero m'Mwambamwamba.","Ndipo Afarisi ena a m'khamu la anthu anati kwa Iye, Mphunzitsi, dzudzulani ophunzira anu.","Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.","Ndipo m'mene anayandikira, anaona mudziwo naulirira,","nanena, Ukadazindikira tsiku ili, inde iwetu zinthu za mtendere! Koma tsopano zibisika pamaso pako.","Pakuti masiku adzakudzera, ndipo adani ako adzakuzingira linga, nadzakuzungulira iwe kwete, nadzakutsekereza ponsepo;","ndipo adzakupasula iwe, ndi ana ako mwa iwe; ndipo sadzasiya mwa iwe mwala wina pa mwala unzake; popeza sunazindikira nyengo ya mayang'aniridwe ako.","Ndipo analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa iwo akugulitsa malonda, nanena nao,","Kwalembedwa, Ndipo nyumba yanga idzakhala nyumba yakupemphera; koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.","Ndipo analikuphunzitsa m'Kachisi tsiku ndi tsiku. Koma ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu a anthu anafunafuna kumuononga Iye;","ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve."]