UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 4.34 kB
["Ndipo pamene analikutuluka Iye m'Kachisi, mmodzi wa ophunzira ake ananena kwa Iye, Mphunzitsi, onani, miyala yotere ndi nyumba yotere.","Ndipo Yesu anati kwa iye, Kodi waona nyumba izi zazikulu? Sudzasiyidwa pano mwala umodzi pamwamba pa unzake, umene sudzagwetsedwa.","Ndipo pamene anakhala Iye pa phiri la Azitona, popenyana ndi Kachisi, anamfunsa Iye m'tseri Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Andrea, kuti,","Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndi chotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pa kumalizidwa zinthu izi zonse?","Ndipo Yesu anayamba kunena nao, Yang'anirani kuti munthu asakusocheretseni.","Ambiri adzafika m'dzina langa, nadzanena, Ine ndine Iye; nadzasocheretsa ambiri.","Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.","Pakuti mtundu wa anthu udzayambana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu unzake: padzakhala zivomezi m'malo m'malo; padzakhala njala; izi ndi zoyambira za zowawa.","Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.","Ndipo Uthenga Wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.","Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.","Ndipo mbale adzapereka mbale wake kuti amuphe, ndi atate mwana wake; ndi ana adzayambana ndi akuwabala, nadzawaphetsa.","Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa: koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, yemweyo adzapulumutsidwa.","Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri:","ndi iye amene ali pamwamba pa chindwi asatsike, kapena asalowe kukatulutsa kanthu m'nyumba mwake;","ndi iye amene ali kumunda asabwere kudzatenga malaya ake.","Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi akuyamwitsa ana masiku awo!","Ndipo pempherani kuti kusakhale m'nyengo yachisanu.","Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse.","Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.","Ndipo pamenepo wina akati kwa inu, Onani Khristu ali pano; kapena, Onani, uko; musavomereze;","pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.","Koma yang'anirani; onani ndakuuziranitu zinthu zonse, zisanafike.","Koma m'masikuwo, chitatha chisautso chimenecho, dzuwa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake,","ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera m'mwamba ndi mphamvu zili m'mwamba zidzagwedezeka.","Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza m'mitambo ndi mphamvu yaikulu, ndi ulemerero.","Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.","Ndipo phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene pafika kuti nthambi yake ikhala yanthete, ndipo anaphuka masamba ake, muzindikira kuti layandikira dzinja;","chomwecho inunso, pamene muona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti ali pafupi pakhomo.","Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika.","Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.","Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, angakhale angelo m'Mwamba, angakhale Mwana, koma Atate ndiye.","Yang'anirani, dikirani, pempherani: pakuti simudziwa nthawi yake.","Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.","Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamawa;","kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m'tulo.","Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani."]