UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.81 kB
["Pamenepo anayandikiza ana akazi a Zelofehadi mwana wa Hefere, ndiye mwana wa Giliyadi, ndiye mwana wa Makiri, ndiye mwana wamwamuna wa Manase, wa mabanja a Manase mwana wa Yosefe; ndipo maina a ana ake akazi ndiwo, Mala, Nowa, Hogila ndi Milika ndi Tiriza.","Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti,","Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana amuna.","Lichotsedwerenji dzina la atate wathu pakati pa banja lake, popeza alibe mwana wamwamuna? Tipatseni dziko lathulathu pakati pa abale a atate wathu.","Ndipo Mose anapita nao mlandu wao pamaso pa Yehova.","Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,","Ana akazi a Zelofehadi anena zoona; uwapatse ndithu cholowa chikhale chaochao pakati pa abale a atate wao; nuwalandiritse cholowa cha atate wao.","Ndipo unene ndi ana a Israele, ndi kuti, Akafa munthu wamwamuna wopanda mwana wamwamuna, cholowa chake achilandire mwana wake wamkazi.","Ndipo akapanda kukhala naye mwana wamkazi, mupatse abale ake cholowa chake.","Ndipo akapanda kukhala nao abale, mupatse abale a atate wake cholowa chake.","Ndipo akapanda abale a atate wake, mupatse wa chibale chake woyandikizana naye wa fuko lake cholowa chake, likhale lakelake; ndipo likhale kwa ana a Israele lemba monga Yehova wamuuza Mose.","Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kwera m'phiri ili la Abarimu, nupenye dziko limene ndapatsa ana a Israele.","Utaliona iwenso udzaitanidwa kunka kwa anthu a mtundu wako, monga anaitanidwa Aroni mbale wako;","popeza munapikisana nao mau anga m'chipululu cha Zini, potsutsana nane khamulo, osandipatula Ine pa madziwo pamaso pao. Ndiwo madzi a Meriba m'Kadesi, m'chipululu cha Zini.","Ndipo Mose ananena ndi Yehova, nati,","Yehova, Mulungu wa mizimu ya anthu onse, aike munthu pa khamulo,","wakutuluka pamaso pao, ndi kulowa pamaso pao, wakuwatulutsa ndi kuwalowetsa; kuti khamu la Ambuye lisakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.","Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;","numuimike pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse; numlangize pamaso pao.","Ndipo umuikirepo ulemerero wako, kuti khamu lonse la ana a Israele ammvere.","Ndipo aime pamaso pa Eleazara wansembe, amene amfunsire monga mwa chiweruzo cha Urimu pamaso pa Yehova; ponena iye azituluka, ndi ponena iye azilowa, ndi iye ndi ana onse a Israele pamodzi naye, ndiwo khamu lonse.","Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza; natenga Yoswa namuimitsa pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa khamu lonse;","namuikira manja ake, namlangiza monga Yehova adanena ndi dzanja la Mose."]