UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 7.84 kB
["Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati,","Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo m'Israele.","Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti,","Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito.","Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu;","Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi.","Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.","Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu.","Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova;","ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro.","Koma sanafe ana amuna a Kora.","Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini;","Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo.","Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri.","Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni;","Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri;","Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli.","Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu.","Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani.","Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera.","Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli.","Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.","Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni;","Yasubu, ndiye kholo la banja la Ayasubu; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi.","Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu.","Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele.","Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.","Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu.","Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi.","Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki;","ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu;","ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere.","Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.","Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.","Ana amuna a Efuremu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekere, ndiye kholo la banja la Abekere; Tahani, ndiye kholo la banja la Atahani.","Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani.","Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao.","Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu;","Sefufamu ndiye kholo la banja la Asefufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu.","Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani.","Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.","Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao.","Mabanja onse a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai.","Ana amuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Imina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya.","Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele.","Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Asere ndiye Sera.","Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Asere monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.","Ana amuna a Nafutali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeele, ndiye kholo la banja la Ayezeele; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;","Yezere, ndiye kholo la banja la Ayezere; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.","Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.","Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.","Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,","Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao.","Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake.","Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao.","Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere.","Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.","Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu.","Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao.","Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni.","Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova.","Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.","Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko.","Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai.","Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni."]