bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.6 kB
JSON
["Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,","Nena ndi ana a Israele, nulandire kwa yense ndodo, banja lililonse la makolo ndodo imodzi, mtsogoleri wa mafuko ao onse monga mwa mabanja a makolo ao azipereka ndodo, zikhale khumi ndi ziwiri; nulembe dzina la yense pa ndodo yake.","Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.","Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu.","Ndipo kudzali, kuti ndodo ya munthu ndimsankheyo, idzaphuka; ndipo ndidzadziletsera madandaulo a ana a Israele amene adandaula nao pa inu.","Ndipo Mose ananena ndi ana a Israele, ndipo akalonga ao onse anapereka, yense ndodo imodzi, monga mwa mabanja a makolo ao, ndodo khumi ndi ziwiri; ndi ndodo ya Aroni inakhala pakati pa ndodo zao.","Ndipo Mose anaika ndodozo pamaso pa Yehova m'chihema cha mboni.","Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose analowa m'chihema cha mboni; ndipo taonani, ndodo ya Aroni, ya pa banja la Levi, inaphuka, nionetsa timaani, nichita maluwa, nipatsa akatungurume.","Ndipo Mose anatulutsa ndodo zonse kuzichotsa pamaso pa Yehova, azione ana onse a Israele; ndipo anapenya, natenga yense ndodo yake.","Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.","Ndipo Mose anachita monga Yehova adamuuza, momwemo anachita.","Pamenepo ana a Israele ananena ndi Mose, nati, Taonani, tikufa, tionongeka, tionongeka tonse.","Yense wakuyandikiza Kachisi wa Yehova amwalira; kodi tidzatha nkufa?"]