bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 871 B
JSON
["Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.","Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.","Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.","Kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga, ndinamlamuliracho m'Horebu chikhale cha Israele lonse, ndicho malemba ndi maweruzo.","Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova.","Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse."]