UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.36 kB
["Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti.","Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha;Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka,pakati pa zaka mudziwitse;pa mkwiyo mukumbukire chifundo.","Mulungu anafuma ku Temani,ndi Woyerayo kuphiri la Parani.Ulemerero wake unaphimba miyamba,ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza.","Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika;anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake,ndi komweko kunabisika mphamvu yake.","Patsogolo pake panapita mliri,ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.","Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi;anapenya, nanjenjemeretsa amitundu;ndi mapiri achikhalire anamwazika,zitunda za kale lomwe zinawerama;mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe.","Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka;nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera.","Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje?Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi,kapena ukali wanu panyanja,kuti munayenda pa akavalo anu,pa magaleta anu a chipulumutso?","Munapombosola uta wanu;malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona.Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje.","Mapiri anakuonani, namva zowawa;chigumula cha madzi chinapita;madzi akuya anamveketsa mau ake,nakweza manja ake m'mwamba.","Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao;pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo.Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.","Munaponda dziko ndi kulunda,munapuntha amitundu ndi mkwiyo.","Munatulukira chipulumutso cha anthu anu,chipulumutso cha odzozedwa anu;munakantha mutu wa nyumba ya woipa,ndi kufukula maziko kufikira m'khosi.","Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake;anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza;kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.","Munaponda panyanja ndi akavalo anu,madzi amphamvu anaunjikana mulu.","Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka,milomo yanga inanthunthumira pamau,m'mafupa mwanga mudalowa chivundi,ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga;kuti ndipumule tsiku lamsauko,pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.","Chinkana mkuyu suphuka,kungakhale kulibe zipatso kumpesa;yalephera ntchito ya azitona,ndi m'minda m'mosapatsa chakudya;ndi zoweta zachotsedwa kukhola,palibenso ng'ombe m'makola mwao;","koma ndidzakondwera mwa Yehova,ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.","Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga,asanduliza mapazi anga ngati a mbawala,nadzandipondetsa pa misanje yanga."]