bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.29 kB
JSON
["Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yona nthawi yachiwiri, ndi kuti,","Nyamuka, pita ku Ninive mudzi waukulu uja, nuulalikire uthenga umene ndikuuza.","Ndipo Yona ananyamuka, napita ku Ninive, monga mwa mau a Yehova. Koma Ninive ndiwo mudzi waukulu pamaso pa Yehova, wa ulendo wa masiku atatu.","Ndipo Yona anayamba kulowa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka.","Ndipo anthu a Ninive anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng'ono wa iwowa.","Pakuti mau awa anafikira mfumu ya Ninive, ndipo inanyamuka kumpando wake wachifumu, nivula chofunda chake, nifunda chiguduli, nikhala m'maphulusa.","Ndipo analalikira, nanena m'Ninive mwa lamulo la mfumu ndi nduna zake, ndi kuti, Ngakhale munthu kapena nyama, ngakhale ng'ombe kapena nkhosa, zisalawe kanthu, zisadye, zisamwe madzi;","koma zifundidwe ndi chiguduli munthu ndi nyama, nizifuulire kolimba kwa Mulungu; ndipo abwere yense kuleka njira yake yoipa, ndi chiwawa chili m'manja mwake.","Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.","Ndipo Mulungu anaona ntchito zao, kuti anabwera kuleka njira yao yoipa; ndipo Mulungu analeka choipa adanenachi kuti adzawachitira, osachichita."]