bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.47 kB
JSON
["Imvani mau a Yehova, inu ana a Israele; pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi okhala m'dziko, popeza palibe choonadi, kapena chifundo, kapena kudziwa Mulungu m'dziko.","Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.","Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.","Koma munthu asatsutsane ndi mnzake, kapena kudzudzula mnzake; popeza anthu ako ndiwo akunga otsutsana ndi wansembe.","Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.","Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.","Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.","Adyerera tchimo la anthu anga, nakhumbira chosalungama chao, yense ndi mtima wake.","Ndipo kudzakhala monga anthu, momwemo wansembe; ndipo ndidzawalanga chifukwa chanjira zao, ndi kuwabwezera machitidwe ao.","Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova.","Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.","Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.","Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo.","Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.","Chinkana iwe, Israele, uchita uhule, koma asapalamule Yuda; ndipo musafika inu ku Giligala, kapena kukwera ku Betaveni, kapena kulumbira, Pali Yehova.","Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.","Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.","Chakumwa chao chasasa, achita uhule kosalekeza; akulu ao akonda manyazi kwambiri.","Mphepo yamkulunga m'mapiko ake, ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zao."]