bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.19 kB
JSON
["Israele, bwerera kunka kwa Yehova Mulungu wako; pakuti wagwa mwa mphulupulu yako.","Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.","Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.","Ndidzachiritsa kubwerera kwao, ndidzawakonda mwaufulu; pakuti mkwiyo wanga wamchokera.","Ndidzakhala kwa Israele ngati mame; adzachita maluwa ngati kakombo, ndi kutambalalitsa mizu yake ngati Lebanoni.","Nthambi zake zidzatambalala, ndi kukoma kwake kudzanga kwa mtengo wa azitona, ndi fungo lake ngati Lebanoni.","Iwo okhala pansi pa mthunzi wake adzabwera, nadzatsitsimuka ngati tirigu, nadzaphuka ngati mpesa, chikumbukiro chake chidzanga vinyo wa Lebanoni.","Efuremu adzati, Ndili ndi chiyaninso ndi mafano? Ndayankha, ndidzampenyerera; ndili ngati mtengo wamlombwa wabiriwiri; zipatso zako zipezeka zochokera kwa Ine.","Wanzeru ndani, kuti azindikire izi? Waluntha, kuti adziwe izi? Pakuti njira za Yehova zili zoongoka; ndipo olungama adzayendamo, koma olakwa adzagwamo."]