UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.66 kB
["Efuremu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse achulukitsa mabodza ndi chipasuko, ndipo achita pangano ndi Asiriya, natenga mafuta kunka nao ku Ejipito.","Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zake, adzambwezera monga mwa machitidwe ake.","M'mimba anagwira kuchitende cha mkulu wake, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu;","inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;","ndiye Yehova Mulungu wa makamu, chikumbukiro chake ndi Yehova.","M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.","Ndiye Mkanani, m'dzanja lake muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa.","Ndipo Efuremu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera chuma m'ntchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala tchimo.","Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako chichokere dziko la Ejipito, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a zikondwerero zoikika.","Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndachulukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo.","Kodi Giliyadi ndiye wopanda pake? Akhala achabe konse; m'Giligala aphera nsembe ya ng'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'michera ya munda.","Ndipo Yakobo anathawira kuthengo la Aramu, ndi Israele anagwira ntchito chifukwa cha mkazi, ndi chifukwa cha mkazi anaweta nkhosa.","Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israele kuchokera m'Ejipito, ndi mwa mneneri anasungika.","Efuremu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wake, ndi Ambuye wake adzambwezera chomtonza chake."]