UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 915 B
["Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,","Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uliwonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?","Kodi atengako mtengo kupanga nao ntchito? Atengako chichiri kodi kupachikapo chipangizo chilichonse?","Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse?","Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse?","Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu.","Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.","Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova."]