UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 3.49 kB
["Pamenepo anafika kwa ine akulu ena a Israele nakhala pansi pamaso panga.","Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,","Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?","Chifukwa chake ulankhule nao, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Aliyense wa nyumba ya Israele wakuutsa mafano ake mumtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadza kwa mneneri, Ine Yehova ndidzamyankhapo monga mwa mafano ake aunyinji;","kuti ndigwire nyumba ya Israele mumtima mwao; popeza onsewo asanduka alendo ndi Ine mwa mafano ao.","Chifukwa chake uziti kwa nyumba ya Israele, Atero Ambuye Yehova, Bwerani, lekani mafano anu, tembenuzani nkhope zanu kuzisiya zonyansa zanu zonse.","Pakuti aliyense wa nyumba ya Israele, kapena wa alendo ogonera m'Israele, wodzisiyanitsa kusatsata Ine, nautsa mafano ake m'mtima mwake, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yake pamaso pake, nadzera mneneri kudzifunsira kwa Ine, Ine Yehova ndidzamyankha ndekha;","ndipo ndidzaikira munthu uyu nkhope yanga imtsutse, ndi kumuyesa chodabwitsa, ndi chizindikiro, ndi mwambi, ndi kumsadza pakati pa anthu anga; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.","Ndipo akacheteka mneneriyo, nakanena mau, Ine Yehova ndamcheta mneneri uja; ndipo ndidzamtambasulira dzanja langa, ndi kumuononga pakati pa anthu anga Israele.","Ndipo adzasenza mphulupulu yao, mphulupulu ya mneneri idzanga mphulupulu ya uja wamfunsira;","kuti nyumba ya Israele isasocherenso kusatsata Ine, kapena kudzidetsanso ndi zolakwa zao zonse; koma kuti akhale anthu anga, ndipo ndikhale Ine Mulungu wao, ati Ambuye Yehova.","Ndipo anandidzera mau a Yehova akuti,","Likandichimwira dziko ndi kuchita monyenga, ndipo ndikalitambasulira dzanja langa, ndi kulithyolera mchirikizo wake, ndiwo mkate, ndi kulitumizira njala, ndi kulidulira munthu ndi nyama,","chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.","Ndikapititsa zilombo zoipa pakati pa dziko, nizipulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,","chinkana anthu omwewo atatu akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; iwo akadapulumuka okha; koma dziko likadakhala lachipululu.","Kapena ndikadza pa dziko ndi lupanga, ndi kuti, Lupanga lipite pakati pa dziko, kuti ndilidulire munthu ndi nyama;","chinkana anthu atatuwo akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; koma iwo akadapulumuka okha.","Kapena ndikatumizira dzikolo mliri, ndi kulitsanulira ukali wanga ndi mwazi, kulidulira munthu ndi nyama;","chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana amuna kapena akazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.","Pakuti atero Ambuye Yehova, Kopambana kotani nanga ndikatumizira Yerusalemu maweruzo anga anai owawa, lupanga, njala, zilombo zoipa, ndi mliri, kuudulira anthu ndi nyama?","Koma onani mudzatsala opulumuka m'mwemo amene adzatulutsidwa, ndiwo ana aamuna ndi aakazi; taonani, adzatuluka kudza kwa inu; ndipo mudzaona njira zao, ndi zochita zao; mudzatonthozedwanso pa zoipa ndazitengera pa Yerusalemu, inde pa zonse ndazitengerapo.","Ndipo adzakusangalatsani pamene muona njira yao, ndi zochita zao; ndipo mudzadziwa kuti sindinazichita kopanda chifukwa zonse ndinazichita momwemo, ati Ambuye Yehova."]