bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.44 kB
JSON
["Yehova, kumbukirani chotigwerachi,penyani nimuone chitonzo chathu.","Cholowa chathu chasanduka cha alendo,ndi nyumba zathu za achilendo.","Ndife amasiye opanda atate,amai athu akunga akazi amasiye.","Tinamwa madzi athu ndi ndalama,tiona nkhuni zathu pozigula.","Otilondola atigwira pakhosi pathu,tatopa osaona popumira.","Tinagwira mwendo Ejipitondi Asiriya kuti tikhute zakudya.","Atate athu anachimwa, kulibe iwo;ndipo tanyamula mphulupulu zao.","Akapolo atilamulira;palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.","Timalowa m'zoopsa potenga zakudya zathu,chifukwa cha lupanga la m'chipululu.","Khungu lathu lapserera ngati pamotochifukwa cha kuwawa kwa njala.","Anaipitsa akazi m'Ziyoni,ndi anamwali m'midzi ya Yuda.","Anawapachika akalonga manja ao;sanalemekeze nkhope za akulu.","Anyamata ananyamula mphero,ana nakhumudwa posenza nkhuni.","Akulu adatha kuzipata,anyamata naleka nyimbo zao.","Chimwemwe cha mtima wathu chalekeka,masewera athu asanduka maliro.","Korona wagwa pamutu pathu;kalanga ife! Pakuti tinachimwa.","Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka,chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;","pa phiri la Ziyoni lopasukaloankhandwe ayendapo.","Inu, Yehova, mukhala chikhalire,ndi mpando wanu wachifumu ku mibadwomibadwo.","Bwanji mutiiwala chiiwalire,ndi kutisiya masiku ambirimbiri.","Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova,ndipo tidzatembenuzidwadi,mukonzenso masiku athu ngati kale lija.","Koma mwatikaniza konse,mwatikwiyira kopambana."]