UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.82 kB
["Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika;miyala ya malo opatulika yakhuthulidwapa malekezero a makwalala onse.","Ana a Ziyoni a mtengo wapatali,olingana ndi golide woyengetsa,angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.","Angakhale ankhandwe amapatsa bere, nayamwitsa ana ao;koma mwana wamkazi wa anthu a mtundu wangawasanduka wankhanza,ngati nthiwatiwa za m'chipululu.","Lilime la mwana woyamwa limamatirakumalakalaka kwake ndi ludzu;ana ang'ono apempha mkate koma palibe wakuwanyemera.","Omwe anadya zolongosoka angosiyidwa m'makwalala;omwe analeredwa navekedwa mlangali afungatira madzala.","Pakuti mphulupulu ya mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga,ikula koposa tchimo la Sodomu,umene unapasuka m'kamphindi, anthu osauchitira kanthu.","Omveka ake anakonzekakoposa chipale chofewa, nayera koposa mkaka,matupi ao anafiira koposa timiyala toti psu;maonekedwe ao ananga a safiro wa mtengo wapatali.","Maonekedwe ao ada koposa makala,sazindikirika m'makwalala;khungu lao limamatira pa mafupa ao,lakhwinyata, lasanduka ngati ndodo.","Ophedwa ndi lupanga amva bwinokupambana ophedwa ndi njala;pakuti amenewa angokwalika napyozedwa,posowa zipatso za m'munda.","Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao;anali chakudya chao poonongekamwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga.","Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake;anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ake.","Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire,ngakhale onse okhala kunja kuno,kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.","Ndicho chifukwa cha machimo a anenerindi mphulupulu za ansembe ake,amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake.","Asochera m'makwalala ngati akhungu,aipsidwa ndi mwazi;anthu sangakhudze zovala zao.","Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu,chokani, chokani, musakhudze kanthu.Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati mwa amitundu,sadzagoneranso kuno.","Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso;iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu.","Maso athu athedwa, tikali ndi moyo,poyembekeza thandizo chabe;kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa.","Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu;chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa;pakuti chitsiriziro chathu chafikadi.","Otilondola anaposa ziombankhangaza m'mlengalenga m'liwiro lao,anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu.","Wodzozedwa wa Yehova,ndiye mpweya wa m'mphuno mwathu,anagwidwa m'maenje ao;amene tinanena kuti,Tidzakhala m'mthunzi mwake pakati pa amitundu,","kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu,wokhala m'dziko la Uzi;chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso;udzaledzera ndi kuvula zako.","Mphulupulu yako yatha, mwana wamkazi wa Ziyoni,Yehova sadzakutenganso ndende;koma adzazonda mphulupulu yako, mwana wa mkazi wa Edomu,nadzavumbulutsa zochimwa zako."]