bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.79 kB
JSON
["Ambuye waphimbatu ndi mtambomwana wamkazi wa Ziyoni, pomkwiyira!Wagwetsa pansi kuchokera kumwambakukoma kwake kwa Israele;osakumbukira poponda mapazi ake tsiku la mkwiyo wake.","Yehova wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni;wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake;wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.","Pokwiya moopsa walikha nyanga zonse za Israele;wabweza m'mbuyo dzanja lake lamanja pamaso pa adaniwo,natentha Yakobo ngati moto wamalawi wonyambita mozungulira.","Wathifula uta wake ngati mdani,waima ndi dzanja lake lamanja ngati mmaliwongo;wapha onse okondweretsa maso;watsanulira ukali wake ngati motopa hema wa mwana wamkazi wa Ziyoni.","Yehova wasanduka mdani, wameza Israele;wameza zinyumba zake zonse, wapasula malinga ake;nachulukitsira mwana wamkazi wa Yuda maliro ndi chibumo.","Wachotsa mwamphamvu dindiro lake ngati la m'munda;waononga mosonkhanira mwake;Yehova waiwalitsa anthu msonkhano ndi Sabata m'Ziyoni;wanyoza mfumu ndi wansembe mokwiya mwaukali.","Ambuye wataya guwa lake la nsembe,malo ake opatulika amnyansira;wapereka m'manja a adani ake makoma a zinyumba zake;iwo anaphokosera m'nyumba ya Yehova ngati tsiku la msonkhano.","Yehova watsimikiza mtima kupasula lingala mwana wamkazi wa Ziyoni;watambalika chingwe, osabweza dzanja lake kuti lisaonongepo;waliritsa tchemba ndi linga; zilefuka pamodzi.","Zipata zake zalowa pansi;waononga ndi kuthyola mipiringidzo yake;mfumu yake ndi akalonga akeali pakati pa amitundu akusowa chilamulo;inde, aneneri ake samalandira masomphenya kwa Yehova.","Akulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi natonthola;aponya fumbi pa mitu yao,anamangirira chiguduli m'chuuno mwao:Anamwali a ku Yerusalemu aweramitsa pansi mitu yao.","Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka;chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasulakwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga;chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mudziwu.","Amati kwa amao, Tirigu ndi vinyo ali kuti?Pokomoka iwo ngati olasidwa m'makwalala a mudziwu,potsanulidwa miyoyo yao pa zifuwa za amao.","Ndikuchitire umboni wotani? Ndikuyerekeze ndi chiyani,mwana wamkazi wa Yerusalemu?Ndikulinganize ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwaliwe,mwana wamkazi wa Ziyoni?Popeza akula ngati nyanja; ndani angakuchize?","Aneneri ako anakuonera masomphenya achabe ndi opusa;osawulula mphulupulu yako kuti abweze undende wako,koma anakuonera manenero achabe ndi opambutsa.","Onse opita panjira akuombera manja:Atsonya, napukusira mitu yaopa mwana wamkazi wa Yerusalemu, nati,kodi uwu ndi mudzi wotchedwa wokongola, wangwiro,wokondweretsa dziko lonse?","Adani ako onse ayasamira pa iwe,atsonya nakukuta mano, nati, Taumeza;ndithu ili ndi tsiku tinaliyembekezalo, talipeza, taliona.","Yehova wachita chomwe analingalira;watsiriza mau ake, amene analamulira nthawi yakale;wagwetsa osachitira chisoni;wakondweretsa adani pa iwe,wakweza nyanga ya amaliwongo ako.","Mtima wao unafuula kwa Ambuye,linga iwe la mwana wamkazi wa Ziyoni,igwe misozi ngati mtsinje usana ndi usiku;usapume kanthawi, asaleke mwana wa diso lako.","Tauka, tafuula usiku, poyamba kulonda;tsanulira mtima wako ngati madzi pamaso pa Ambuye;takwezera maso ako kwa Iye, chifukwa cha moyo wa tiana tako,timene tilefuka ndi njala pa malekezero a makwalala onse.","Onani Yehova, nimupenye, mwachitira ayani ichi?Kodi akazi adzadya zipatso zao,kunena ana amene anawalera wokha?Kodi wansembe ndi mneneri adzaphedwam'malo opatulika a Ambuye?","Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala;anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga;munawapha tsiku la mkwiyo wanu,munawagwaza osachitira chisoni.","Mwaitana zondiopsa mozungulira ngati tsiku la msonkhano;panalibe wopulumuka ndi wotsala tsiku la mkwiyo wa Yehova;omwe ndinawaseweza ndi kuwalera, adaniwo anawatsiriza."]