bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.66 kB
JSON
["Ha! Mudziwo unadzala anthu, ukhalatu pa wokha!Ukunga mkazi wamasiye!Waukuluwo mwa amitundu, kalonga wamkazi m'madera a dzikowasanduka wolamba!","Uliralira usiku; misozi yake ili pa masaya ake;mwa onse amene anaukonda mulibe mmodzi wakuutonthoza:Mabwenzi ake onse auchitira ziwembu,asanduka adani ake.","Yuda watengedwa ndende chifukwa cha msauko ndi ukapolo waukulu;akhala mwa amitundu, sapeza popuma;onse akumlondola anampeza pakati popsinjikiza.","M'njira za Ziyoni mulira posoweka akudzera msonkhano;pa zipata zake zonse papasuka; ansembe ake onse ausa moyo;anamwali ake asautsidwa; iye mwini namva zowawa.","Amaliwongo ake asanduka akulu ake, adani ake napindula;pakuti Yehova wamsautsa pochuluka zolakwa zake;ana ake ang'ono alowa m'ndende pamaso pa adani ake.","Ulemu wake wonse wamchokera mwana wamkazi wa Ziyoni;akalonga ake asanduka nswala zosapeza busa,anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompirikitsa.","M'masiku a msauko wake ndi kusochera kwakeYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zake zonse zachikhalire;pogwidwa anthu ake ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,mdaniwo anamuona naseka mwachipongwe mabwinja ake.","Yerusalemu wachimwa kwambiri;chifukwa chake wasanduka chinthu chonyansa;onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamaliseche;inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.","Udyo wake unali m'nsalu zake;sunakumbukira chitsiriziro chake;chifukwa chake watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;taonani, Yehova, msauko wanga,pakuti mdaniyo wadzikuza yekha.","Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse;pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika,amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.","Anthu ake onse ausa moyo nafunafuna mkate;ndi zokondweretsa zao agula zakudyakuti atsitsimutse moyo wao;taonani, Yehova, nimupenye;pakuti ndasanduka wonyansa.","Kodi muyesa chimenechi chabe,nonsenu opita panjira?Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni chinangati changachi amandimvetsa ine,chimene Yehova wandisautsa nachotsiku la mkwiyo wake waukali?","Anatumiza moto wochokera kumwambakulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa;watchera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo;wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.","Goli la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lake;zalukidwa, zakwera pakhosi panga;iye wakhumudwitsa mphamvu yanga;Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.","Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga;waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga,Ambuye wapondereza namwaliyo,mwana wamkazi wa Yuda,monga mopondera mphesa.","Chifukwa cha zimenezi ndilira;diso langa, diso langatu likudza madzi:Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira;ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.","Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza;Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake;Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.","Yehova ali wolungama;pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwake;mumvetu, mitundu ya anthu nonsenu,nimuone chisoni changa;anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.","Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga;ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mudzimu,alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.","Onani, Yehova; pakuti ndavutika,m'kati mwanga mugwedezeka;mtima wanga wasanduka mwa ine;pakuti ndapikisana nanu ndithu;kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.","Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza;adani anga onse atha kumva msauko wanga,nakondwera kuti mwatero ndinu;mudzafikitsa tsiku lija mwalitchula,ndipo iwowo adzanga ine.","Zoipa zao zonse zidze pamaso panu,muwachitire monga mwandichitira inechifukwa cha zolakwa zanga zonse,pakuti ndiusa moyo kwambiri,ndi kulefuka mtima wanga."]