UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 967 B
["Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.","Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kutuluka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse zili m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.","Pomveka migugu ya ziboda za olimba ake, pogumukira magaleta ake, ndi pophokosera njinga zake, atate sadzacheukira ana ao chifukwa cha kulefuka kwa manja ao;","chifukwa cha tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Tiro ndi Sidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a chisumbu cha Kafitori.","Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'chidikha chao; udzadzicheka masiku angati?","Iwe lupanga la Yehova, atsala masiku angati osakhala chete iwe? Dzilonge wekha m'chimake; puma, nukhale chete.","Udzakhala chete bwanji, popeza Yehova anakulangiza? Za Asikeloni, ndi za m'mphepete mwa nyanja, pamenepo analiika."]