UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.12 kB
["Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,","pamenepo ananena Azariya mwana wake wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumize iwe kudzanena, Musalowe m'Ejipito kukhala m'menemo;","koma Baruki mwana wake wa Neriya atichichizira inu, mutipereke m'dzanja la Ababiloni, kuti atiphe ife, atitengere ife am'nsinga ku Babiloni.","Ndipo Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, ndi anthu onse sanamvere mau a Yehova, kuti akhale m'dziko la Yuda.","Koma Yohanani mwana wake wa Kareya, ndi akazembe onse a nkhondo, anatenga otsala onse a Yuda, amene anabwera kumitundu yonse kumene anaingitsidwirako kuti akhale m'dziko la Yuda;","ndi amuna, ndi akazi, ndi ana, ndi ana akazi a mfumu, ndi anthu onse amene Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya ndi Gedaliya mwana wake wa Ahikamu, mwana wake wa Safani, ndi Yeremiya mneneri, ndi Baruki mwana wake wa Neriya;","ndipo anadza nalowa m'dziko la Ejipito; pakuti sanamvere mau a Yehova; ndipo anadza mpaka ku Tapanesi.","Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yeremiya m'Tapanesi, kuti,","Tenga miyala yaikulu m'dzanja lako, nuiyale ndi dothi pakati pa njerwa, za pa khomo la nyumba ya Farao m'Tapanesi pamaso pa anthu a Yuda;","ndi kuti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani Ine ndidzatuma ndidzatenga Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, mtumiki wanga, ndi kuika mpando wake wachifumu pa miyalayi ndaiyala; ndipo iye adzaivundikira ndi hema wachifumu wake.","Ndipo iye adzafika, nadzakantha dziko la Ejipito; nadzapereka kuimfa iwo a kuimfa, ndi kundende iwo a kundende, ndi kulupanga iwo a kulupanga.","Ndidzayatsa moto m'nyumba za milungu ya Ejipito; ndipo adzazitentha, nadzaitenga ndende; ndipo adzadzifunda ndi dziko la Ejipito, monga mbusa avala chovala chake; nadzatuluka m'menemo ndi mtendere.","Ndipo adzathyola mizati ya zoimiritsa za Kachisi wa dzuwa, ali m'dziko la Ejipito; ndi nyumba za milungu ya Aejipito adzazitentha ndi moto."]