bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 4.84 kB
JSON
["Amenewa ndi mau a kalata uja anatumiza Yeremiya mneneri kuchokera ku Yerusalemu kunka kwa akulu otsala a m'nsinga, ndi kwa ansembe, ndi kwa aneneri, ndi kwa anthu onse, amene Nebukadinezara anawatenga ndende ku Yerusalemu kunka ku Babiloni;","anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,","anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,","Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero, kwa am'nsinga onse, amene ndinawatenga ndende ku Yerusalemu kunka nao ku Babiloni:","Mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zake;","tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.","Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.","Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.","Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.","Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.","Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.","Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.","Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.","Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupirikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.","Pakuti mwati, Yehova watiutsira ife aneneri m'Babiloni.","Pakuti Yehova atero za mfumu imene ikhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi za anthu onse amene akhala m'mudzi uno, abale anu amene sanatulukire pamodzi ndi inu kundende;","Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatuma pa iwo lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzayesa iwo onga nkhuyu zoola, zosadyeka, pokhala nzoipa.","Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;","chifukwa sanamvere mau anga, ati Yehova, amene ndinawatumizira ndi atumiki anga aneneri, ndi kuuka mamawa ndi kuwatuma, koma munakana kumva, ati Yehova.","Pamenepo tamvani inu mau a Yehova, inu nonse a m'ndende, amene ndachotsa m'Yerusalemu kunka ku Babiloni.","Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;","ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaocha m'moto;","chifukwa anachita zopusa m'Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.","Ndipo za Semaya Mnehelamu uzinena, kuti,","Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,","Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.","Ndipo tsopano, walekeranji kumdzudzula Yeremiya wa ku Anatoti, amene amadziyesa mneneri wanu,","popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?","Ndipo Zefaniya wansembe anawerenga kalata amene m'makutu a Yeremiya mneneri.","Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, akuti,","Uwatumizire mau am'nsinga onse, akuti, Atero Yehova za Semaya Mnehelamu: Chifukwa Semaya wanenera kwa inu, koma Ine sindinamtuma, ndipo anakukhulupiritsani zonama;","chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova."]