bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.35 kB
JSON
["Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Zedekiya mfumu anatuma kwa iye Pasuri mwana wa Malikiya, ndi Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, akati,","Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.","Ndipo Yeremiya anati kwa iwo, Muzitero kwa Zedekiya:","Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu.","Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi m'ukali waukulu.","Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mudzi uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi chaola chachikulu.","Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi chaola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.","Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.","Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.","Pakuti ndaika nkhope yanga pa mudzi uwu ndiuchitire choipa, si chabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzautentha ndi moto.","Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:","Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.","Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?","Ndipo ndidzakulangani inu monga mwa chipatso cha ntchito zanu, ati Yehova; ndipo ndidzayatsa moto m'nkhalango mwake, ndipo udzatha zonse zomzungulira iye."]