UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2.68 kB
["Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.","Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ochita chilungamo, osasiya chilangizo cha Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.","Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? Ndi bwanji ife tavutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza antchito anu onse.","Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba.","Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? Tsiku lakuvutitsa munthu moyo wake? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wake monga bango, ndi kuyala chiguduli ndi phulusa pansi pake? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lovomerezeka kwa Yehova?","Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?","Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?","Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kuchira kwako kudzaonekera msangamsanga; ndipo chilungamo chako chidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wotchinjiriza pambuyo pako.","Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,","ndipo ngati upereka kwa wanjala chimene moyo wako umakhumba, ndi kukhutitsa moyo wovutidwa, pomwepo kuunika kwako kudzauka mumdima, ndipo usiku wako udzanga usana;","ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.","Ndipo iwo amene adzakhala a iwe adzamanga malo akale abwinja; udzautsa maziko a mibadwo yambiri; udzatchedwa Wokonza pogumuka, Wakubwezera njira zakukhalamo.","Ukaletsa phazi lako pa Sabata, ndi kusiya kuchita kukondwerera kwako tsiku langa lopatulika, ndi kuyesa Sabata tsiku lokondwa lopatulika la Yehova, lolemekezeka, ndipo ukalilemekeza ilo, osachita njira zako zokha, osafuna kukondwa kwako kokha, osalankhula mau ako okha;","pomwepo udzakondwa mwa Yehova; ndipo Ine ndidzakuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi; ndipo ndidzakudyetsa cholowa cha kholo lako Yakobo; pakuti pakamwa pa Yehova pananenapo."]