UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 2 kB
["Ndani wamvera uthenga wathu? Ndi mkono wa Yehova wavumbulukira yani?","Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.","Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeza.","Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu; koma ife tinamuyesa wokhomedwa, wokanthidwa ndi Mulungu, ndi wovutidwa.","Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.","Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.","Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.","Anachotsedwa ku chipsinjo ndi chiweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wake? Pakuti walikhidwa kunja kuno; chifukwa cha kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.","Ndipo anaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yake, ngakhale Iye sanachite chiwawa, ndipo m'kamwa mwake munalibe chinyengo.","Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.","Iye adzaona zotsatira mavuto a moyo wake, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.","Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa."]