bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.01 kB
JSON
["Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya chakudya chathuchathu ndi kuvala zovala zathuzathu; koma titchedwe dzina lako; chotsa chitonzo chathu.","Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.","Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu adzatchedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu;","pamene Ambuye adzasambitsa litsiro la ana akazi a Ziyoni, nadzatsuka mwazi wa Yerusalemu, kuchokera pakatipo, ndi mzimu wa chiweruziro, ndi mzimu wakutentha.","Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse pa phiri la Ziyoni, ndi pa masonkhano ake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.","Ndipo padzakhala chihema cha mthunzi, nthawi ya usana yopewera kutentha, pothawira ndi pousa mvula ndi mphepo."]