UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 3.13 kB
["Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwa; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.","Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, chipulumutso chathunso m'nthawi ya mavuto.","Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iwe amitundu abalalika.","Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga dzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.","Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi chiweruzo ndi chilungamo.","Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.","Taonani, olimba mtima ao angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.","Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asiriya wathyola chipangano, wanyoza midzi, sasamalira anthu.","Dziko lirira maliro ndi kulefuka; Lebanoni ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi chipululu; pa Basani ndi Karimele papukutika.","Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.","Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumalizani inu.","Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.","Imvani inu amene muli kutali, chimene ndachita ndi inu; amene muli pafupi, vomerezani mphamvu zanga.","Ochimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto wakunyeketsa? Ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zachikhalire?","Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;","iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.","Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwake; iwo adzaona dziko lakutali.","Mtima wako udzaganizira zoopsa; mlembi ali kuti? Ali kuti iye amene anayesa msonkho? Ali kuti iye amene anawerenga nsanja?","Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve.","Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa zikondwerero zathu; maso ako adzaona, Yerusalemu malo a phee, chihema chimene sichidzasunthidwa, zichiri zake sizidzazulidwa konse, zingwe zake sizidzadulidwa.","Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.","Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.","Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.","Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao."]