UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.06 kB
["Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.","Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.","Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;","momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.","Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, chifukwa cha Kusi, amene anawatama, ndi Ejipito, amene anawanyadira.","Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?"]