bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 3.52 kB
JSON
["Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.","Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.","Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.","Ndipo ndidzapereka Ejipito m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.","Ndipo madzi adzaphwa m'nyanja yaikulu, ndipo nyanja yoyendamo madzi idzaphwa, niuma.","Ndipo nyanja zidzanunkha; mitsinje ya Ejipito idzachepa, nuima; bango ndi mlulu zidzafota.","Madambo oyandikana ndi Nailo, pafupi ndi gombe la Nailo, ndi zonse zobzala pa Nailo zidzauma, nizichotsedwa, zosakhalanso konse.","Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza m'Nailo adzaliralira, ndi onse oponya makoka m'madzi, adzalefuka.","Komanso iwo amene agwira ntchito yakupala thonje, ndi iwo amene aomba nsalu yoyera, adzakhala ndi manyazi.","Ndipo maziko ake adzasweka, onse amene agwira ntchito yolipidwa adzavutidwa mtima.","Akalonga a Zowani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?","Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito.","Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake.","Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.","Ejipito sadzakhala ndi ntchito, imene mutu pena mchira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.","Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.","Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Ejipito, yense wakulitchula adzamtembenukira mwamantha, chifukwa cha uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.","Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mudzi wa chionongeko.","Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Ejipito, ndi choimiritsa cha Yehova m'malire ake.","Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.","Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.","Ndipo Yehova adzakantha Ejipito kukantha ndi kuchiritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawachiritsa.","Tsiku limenelo padzakhala khwalala lochokera m'Ejipito kunka ku Asiriya, ndipo Mwasuri adzafika ku Ejipito, ndi Mwejipito adzafika ku Asiriya, ndipo Aejipito adzapembedzera pamodzi ndi Aasiriya.","Tsiku limenelo Israele ndi Ejipito ndi Asiriya atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi;","pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa."]