bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.34 kB
JSON
["Ha, dziko lakukupuza mapiko, lili tsidya lija la nyanja za Etiopiya;","limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!","Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.","Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m'kutentha kwa masika.","Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kutcha, iye adzadzombolera tinthambi ndi chikwakwa, ndi nthambi zotasa adzazichotsa ndi kuzisadza.","Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.","Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni."]