bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.17 kB
JSON
["Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wachotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa.","Midzi ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.","Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.","Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lake kudzaonda.","Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.","Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.","Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wake, ndipo maso ake adzalemekeza Woyera wa Israele.","Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.","Tsiku limenelo midzi yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.","Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;","tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwake; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la chisoni chothetsa nzeru.","Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene afuula ngati kukukuma kwa nyanja; ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamanga kwa madzi amphamvu!","Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.","Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanake, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu."]