UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 4.17 kB
["Pakuti Ambuye adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.","Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.","Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa,","pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!","Yehova wathyola mkunkhu wa woipa, ndodo yachifumu ya wolamulira.","Wokantha anthu mwaukali kuwakantha chikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.","Dziko lonse lapuma, lili duu; iwo ayamba kuimba nyimbo.","Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebanoni, ndi kunena, Chigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.","Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.","Onse adzavomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? Kodi iwe wafanana nafe?","Chifumu chako chatsitsidwa kunsi kumanda, ndi phokoso la mingoli yako; mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.","Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!","Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba pa phiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;","ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.","Koma udzatsitsidwa kunsi kumanda, ku malekezero a dzenje.","Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;","amene anapululutsa dziko, napasula midzi yake, amene sanamasule ndende zake, zinke kwao?","Mafumu onse a mitundu, onsewo agona m'ulemerero yense kunyumba kwake.","Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.","Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ochita zoipa sidzatchulidwa konse.","Konzani inu popherapo ana ake, chifukwa cha kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzuka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi midzi.","Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.","Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu.","Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala;","kuti Ine ndidzathyola Asiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pao.","Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.","Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?","Chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.","Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.","Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.","Lira, chipata iwe; fuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake.","Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira."]