bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 699 B
JSON
["Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.","Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.","Chifukwa chake mudzakondwera pakutunga madzi m'zitsime za chipulumutso.","Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa.","Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero; chidziwike ichi m'dziko lonse.","Tafuula, takuwa iwe, wokhala m'Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu."]