bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 4.02 kB
JSON
["Masomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.","Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.","Ng'ombe idziwa mwini wake, ndi bulu adziwa pomtsekereza: koma Israele sadziwa, anthu anga sazindikira.","Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.","Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.","Kuchokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe changwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zilonda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.","Dziko lanu lili bwinja; midzi yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.","Ndipo mwana wamkazi wa Ziyoni wasiyidwa ngati chitando cha m'munda wamphesa, chilindo cha m'munda waminkhaka, ngati mudzi wozingidwa ndi nkhondo.","Akadapanda Yehova wa makamu kutisiyira otsala ang'onong'ono ndithu, ife tikanakhala ngati Sodomu, ife tikadanga Gomora.","Imvani mau a Yehova inu olamulira a Sodomu, tcherani makutu ku chilamulo cha Mulungu wathu, inu anthu a Gomora.","Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.","Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?","Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.","Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.","Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.","Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa;","phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.","Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.","Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,","koma ngati mukana ndi kupanduka, mudzathedwa ndi lupanga; chifukwa m'kamwa mwa Yehova mwatero.","Mudzi wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.","Siliva wako wasanduka mphala, vinyo wako wasanganizidwa ndi madzi.","Akulu ako apanduka, ali anzao a mbala; onse akonda mitulo, natsata zokometsera milandu; iwo saweruzira amasiye; ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye suwafika.","Chifukwa chake Yehova ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;","ndipo ndidzaikanso dzanja langa pa iwe, ndi kukusungunula kukusiyanitsa iwe ndi mphala yako, ndipo ndidzachotsa seta wako wonse:","ndidzabweza oweruza ako monga poyamba, ndi aphungu ako monga pachiyambi; pambuyo pake udzatchedwa Mudzi wolungama, mudzi wokhulupirika.","Ziyoni adzaomboledwa ndi chiweruzo, ndi otembenuka mtima ake ndi chilungamo.","Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.","Chifukwa adzakhala ndi manyazi, chifukwa cha mitengo yathundu munaikhumba, ndipo inu mudzagwa nkhope, chifukwa cha minda imene mwaisankha.","Chifukwa mudzakhala ngati mtengo wathundu, umene tsamba lake linyala, ngatinso munda wopanda madzi.","Ndimo wamphamvu adzakhala ngati chingwe chathonje, ndi ntchito yake ngati nthethe; ndipo zonse zidzayaka moto pamodzi, opanda wozimitsa."]