UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.45 kB
["Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata,mwana wamkaziwe wa mfumu!Pozinga m'chuuno mwako pakunga zonyezimira,ntchito ya manja a mmisiri waluso.","Pamchombo pako pakunga chikho choulungika,chosasowamo vinyo wosanganika:Pamimba pako pakunga mulu wa tiriguwozingidwa ndi akakombo.","Mawere ako akunga ana awiri a nswalaanabadwa limodzi.","Khosi lako likunga nsanja yaminyanga;maso ako akunga matawale a ku Hesiboni,a pa chipata cha Batirabimu;mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebanoniimene iloza ku Damasiko.","Mutu wako ukunga Karimele,ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsalu yofiirira;mfumu yamangidwa ndi nkhata zake ngati wam'nsinga.","Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika,bwenziwe, m'zokondweretsa!","Msinkhu wakowu ukunga mgwalangwa,mawere ako akunga matsango amphesa.","Ndinati, Ndikakwera pa mgwalangwapo,ndikagwira nthambi zake:Mawere ako ange ngati matsango amphesa,ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula.","M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa,womeza tseketseke bwenzi langa,wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.","Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo,ndine amene andifunayo.","Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda;titsotse m'milaga.","Tilawire kunka kuminda yamipesa;tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso,makangaza ndi kutuwa maluwa ake;pompo ndidzakupatsa chikondi changa.","Mankhwala a chikondi anunkhira,ndi pamakomo pathu zipatso zabwino,za mitundumitundu, zakale ndi zatsopano,zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga."]