bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 2.11 kB
JSON
["Ndalowa m'munda mwanga, mlongo wanga, mkwatibwi:Ndatchera mure wanga ndi zonunkhiritsa zanga;ndadya uchi wanga ndi chisa chake;ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.Idyani, atsamwalinu,imwani, mwetsani chikondi.","Ndinagona tulo, koma mtima wanga unali maso:Ndi mau a bwenzi langa mnyamatayo agogoda, nati,nditsegulire, mlongo wanga, wokondedwa wanga,nkhunda yanga, wangwiro wanga:Pakuti pamtu panga padzala mame,patsitsi panga pali madontho a usiku.","Ndinayankha kuti, Ndavula malaya anga, ndiwavalenso bwanji?Ndasuka mapazi anga; ndiwadetserenji?","Bwenzi langa analonga dzanja lake pazenera,mtima wanga ndi kuguguda chifukwa cha iye.","Ndinauka ndikatsegulire bwenzi langa;pamanja panga panakha mure.Ndi pa zala zanga madzi a mure,pa zogwirira za mpikizo.","Ndinamtsegulira bwenzi langalo;koma ndinampeza, bwenzi langa atachoka.Moyo wanga unalefuka polankhula iye:Ndinamfunafuna, osampeza;ndinamuitana, koma sanandivomere.","Alonda akuyenda m'mudzi anandipeza,nandikantha, nanditema;osunga makoma nandichotsera chophimba changa.","Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,mukapeza bwenzi langa, mudzamuuza chiyani?Kuti ndadwala ndi chikondi.","Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,mkaziwe woposa kukongola?Bwenzi lako aposa abwenzi ena bwanji,kuti utilumbirira motero?","Wokondedwa wanga ali woyera ndi wofiira,womveka mwa zikwi khumi.","Mutu wake ukunga golide, woyengetsa,tsitsi lake lopotana, ndi lakuda ngati khungubwi.","Ana a maso ake akunga nkhundapambali pa mitsinje ya madzi;otsukidwa ndi mkaka, okhala pa mitsinje yodzala.","Masaya ake akunga chitipula chobzalamo ndiwo,ngati mitumbira yoyangapo masamba onunkhira:Milomo yake ikunga akakombo, pakukhapo madzi a mure.","Manja ake akunga zing'anda zagolidezoikamo zonyezimira zoti biriwiri.Thupi lake likunga chopanga cha minyangacholemberapo masafiro.","Miyendo yake ikunga zoimiritsa za mwala wonyezimira,zogwirika m'kamwa mwa golide:Maonekedwe ake akunga Lebanoni,okometsetsa ngati mikungudza.","M'kamwa mwake muli mokoma; inde,ndiye wokondweretsa ndithu.Ameneyu ndi wokondedwa wanga,ameneyu ndi bwenzi langa,ana akazi inu a ku Yerusalemu."]