UNPKG

bible-chichewa

Version:

The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.

1 lines 1.39 kB
["Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda:Ndinamfunafuna, koma osampeza.","Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi,m'makwalala ndi m'mabwalo ake,ndimfunefune amene moyo wanga umkonda:Ndimfunafuna, koma osampeza.","Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza:Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?","Nditawapitirira pang'ono,ndinampeza amene moyo wanga umkonda:Ndinamgwiriziza, osamfumbatula,mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai,ngakhale m'chipinda cha wondibala.","Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,pali mphoyo, ndi mbawala ya kuthengo,kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,mpaka chikafuna mwini.","Ndaniyu akwera kutuluka m'chipululu ngati utsi wa tolo,wonunkhira ndi mure ndi lubani,ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?","Taonani, ndi machila a Solomoni;pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi,a mwa ngwazi za Israele.","Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo:Yense ali ndi lupanga lake pantchafu pake,chifukwa cha upandu wa usiku.","Solomoni mfumu anadzipangira machila okhalamo tsongandi matabwa a ku Lebanoni.","Anapanga timilongoti take ndi siliva,cha pansi pake ndi golide, mpando wake ndi nsalu yofiirira,pakati pake panayalidwa za chikondicha ana akazi a ku Yerusalemu.","Tulukani, ana akazi inu a Ziyoni,mupenye Solomoni mfumu,ndi korona amake amamveka naye tsiku la ukwati wake,ngakhale tsiku lakukondwera mtima wake."]