bible-chichewa
Version:
The Chichewa Bible npm package is an open source project that provides developers with a convenient way to access and work with the Chichewa translation of the Bible within their Node.js applications.
1 lines • 1.78 kB
JSON
["Ndine duwa lofiira la ku Saroni,ngakhale kakombo wa kuzigwa.","Ngati kakombo pakati pa mingamomwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.","Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango,momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna.Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wake,zipatso zake zinatsekemera m'kamwa mwanga.","Anandifikitsa kunyumba ya vinyo,mbendera yake yondizolimira inali chikondi.","Mundilimbikitse ndi mphesa zouma,munditonthoze mtima ndi maula,pakuti ndadwala ndi chikondi.","Dzanja lake lamanzere anditsamiritse kumutu,dzanja lake lamanja ndi kundifungatira.","Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu,pali mphoyo, ndi mbawala za kuthengo,kuti musautse, ngakhale kugalamutsa chikondi,mpaka chikafuna mwini.","Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza,alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.","Wokondedwa wanga akunga mphoyo,pena mwana wa mbawala:Taona, aima patseri pakhoma lathu.Apenyera pazenera,nasuzumira pamade.","Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine,tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.","Pakuti, taona, chisanu chatha,mvula yapita yaleka;","maluwa aoneka pansi;nthawi yoimba mbalame yafika,mau a njiwa namveka m'dziko lathu.","Mkuyu utchetsa nkhuyu zake zosakhwima,mipesa niphuka,inunkhira bwino.Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.","Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe,mobisika motsetsereka,ndipenye nkhope yako, ndimve mau ako;pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.","Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono,amene akuononga minda yamipesa;pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.","Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wake:aweta zake pakati akakombo.","Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyopena mwana wa mbawalapa mapiri a mipata."]